Genii Blakk - Mkazi Wapabala

Ndaona ubwino wa mkazi wapabala
Ngakhale amunene kuti ndi mambala
Ubwino wache ndauziwa eh
Ona ubwino wa mkazi wapabala
Ngakhale amunene kuti ndi mambala
Ubwino wake ndauziwa eh

Ndimamvana ndi mkazi wapabala
Samanyada ndi nkhani ya komwe iye amakhala
Samatengera looks kapena zomwe umavala
Simunthu wamba chabe naye anamva kuwawa
Amachezeka bwino ukamtenga bho
Zakwanu m'tembo kwathu m'tembo
Amati zausilu no
Wakumana ndi ziphinjo so chibwana ndipa zero
Kukuchenjeza ikalakwa ngati mu njira simuli bwino
Ndipo, ulusi wake amaponya wa khenge
Kutelela pamalo ngati pagwera denje
Nabola azisake kuti mawa amede
Zikoli ndi latonse bolani kangachepe eh

Ndaona ubwino wa mkazi wapabala
Ngakhale amunene kuti ndi mambala
Ubwino wache ndauziwa eh
Ona ubwino wa mkazi wapabala
Ngakhale amunene kuti ndi mambala
Ubwino wake ndauziwa eh

Ndimamvana ndi mkazi wapabala
Amandilesa kupeza mkazi wachisawawa
Uzakhumudwa nthenda ili ndi am'mipandawa
Magwiragwira mphwanga uzamva nawo kuwawa eh
Timamvana pa nkhaniso ya bawa
Samafuna ziwawa bola azisangalala
Amandithoka zoba ndi yemwe timamukawa
Life is too short time yatha zivaya eh
Sikuti naye safuna chikondi
Chinamuluma chakuda koma ndi wachikondi
Kudyesa ana ake Mpakana abale ake
Olo ena amunene iye amapanga zake eh

Ndaona ubwino wa mkazi wapabala
Ngakhale amunene kuti ndi mambala
Ubwino wache ndauziwa eh
Ona ubwino wa mkazi wapabala
Ngakhale amunene kuti ndi mambala
Ubwino wake ndauziwa eh

Amati zonse ndizotheka aise
Amati zonse ndizotheka aise nabola golide
Amati zonse ndizotheka aise
Amati zonse ndizotheka aise nabola golide
Sinkhani yomakambira kumbali
Kusochera kulipo m'manja mwako muli nyali
Kumayesa kudekha poyang'ana anamwali
Azapezeka easy aise zonse ndi nthawi
Amavutika chonchi kamba ka umphawi
Ufulu ndi mtendele umasowa mwa amayi
Apanga bwanji nanga game ili m'manja mwake
Bola lalero liduse iye atapanga zake eh

Ndaona ubwino wa mkazi wapabala
Ngakhale amunene kuti ndi mambala
Ubwino wache ndauziwa eh
Ona ubwino wa mkazi wapabala
Ngakhale amunene kuti ndi mambala
Ubwino wake ndauziwa eh
Ubwino wa mkazi wapabala
Ngakhale amunene kuti ndi mambala
Ubwino wache ndauziwa eh
Ona ubwino wa mkazi wapabala
Ngakhale amunene kuti ndi mambala
Ubwino wake ndauziwa eh

Yeah, DMG we keep it real all day
DMG we keep it real all day

Written by:
Daniel Mkwezalamba, Neppier Longwe

Publisher:
Lyrics © O/B/O DistroKid

Lyrics powered by Lyric Find

Genii Blakk

View Profile
The Music Man The Music Man